Yeremiya 1:15 - Buku Lopatulika15 Pakuti taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wachifumu wake pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa mizinda yonse ya Yuda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Pakuti taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wachifumu wake pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa midzi yonse ya Yuda. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Ndikuitana anthu a mafuko onse a maufumu akumpoto,” akuterotu Chauta. “Mafumu ao adzabwera, aliyense adzaika mpando wake waufumu pa zipata za Yerusalemu, ndiponso pozungulira malinga ake. Iwo adzazinganso mizinda yonse ya Yuda. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Ine ndikuyitana anthu onse a ku maufumu a kumpoto,” akutero Yehova. “Mafumu awo adzabwera ndipo aliyense adzakhazika mpando wake waufumu polowera pa zipata za Yerusalemu; iwo adzabwera ndi kuzungulira makoma ake ndiponso midzi yonse ya dziko la Yuda. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.