Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yakobo 4:1 - Buku Lopatulika

1 Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Kodi nkhondo zimachokera kuti? Kukangana pakati panu kumachokera kuti? Kodi suja zimachokera ku zilakolako zanu zathupi, zimene zimachita nkhondo mwa inu?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Nʼchiyani chimene chimayambitsa ndewu ndi mapokoso pakati panu? Kodi sizichokera ku zilakolako zimene zimalimbana mʼkati mwanu?

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 4:1
24 Mawu Ofanana  

Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?


Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;


Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.


koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la uchimo m'ziwalo zanga.


Pakuti pamene tinali m'thupi, zilakolako za machimo, zimene zinali mwa chilamulo, zinalikuchita m'ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso.


Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero.


Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.


Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;


Koma mafunso opusa ndi opanda malango upewe, podziwa kuti abala ndeu.


Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.


koma pewa mafunso opusa, ndi mawerengedwe a mibadwo, ndi ndeu, ndi makani a pamalamulo; pakuti sizipindulitsa, ndipo zili zachabe.


koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, ndikumnyenga.


Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.


monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu;


Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;


Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;


ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa