Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yakobo 3:8 - Buku Lopatulika

8 koma lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; lili choipa chotakataka, lodzala ndi ululu wakupha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 koma lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; lili choipa chotakataka, lodzala ndi ululu wakupha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma lilime palibe munthu amene angathe kuliŵeta. Ndi loipa, silidziŵa kupumula, ndipo ndi lodzaza ndi ululu wakupha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 koma palibe munthu amene angaweta lilime. Lilime ndipo silitha kupuma, ndi lodzaza ndi ululu wakupha.

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 3:8
13 Mawu Ofanana  

Anola lilime lao ngati njoka; pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.


Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.


Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.


Ululu wao ukunga wa njoka; akunga mphiri yogontha m'khutu, itseka m'khutu mwake.


Onani abwetuka pakamwa pao; m'milomo mwao muli lupanga, pakuti amati, Amva ndani?


Wokhota mtima sadzapeza bwino; ndipo mwini lilime lokhota adzagwa m'zoipa.


Njoka ikaluma isanalodzedwe, watsenga saona mphotho.


M'mero mwao muli manda apululu; ndi lilime lao amanyenga; ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao;


Vinyo wao ndiwo ululu wa zinjoka, ndi ululu waukali wa mphiri.


Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.


Pakuti mtundu uliwonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa zam'nyanja, zimazoloweretsedwa, ndipo zazoloweretsedwa ndi anthu;


Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa