Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yakobo 2:23 - Buku Lopatulika

23 ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Motero zidachitikadi zimene Malembo adaanena, kuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, nchifukwa chake Mulungu adamuwona kuti ngwolungama;” mwakuti ankatchedwa bwenzi la Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Ndipo Malemba akunena kuti, “Abrahamu anakhulupirira Mulungu ndipo anatengedwa kukhala wolungama,” ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 2:23
22 Mawu Ofanana  

Ndipo anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye chilungamo.


ndi Azariya mwana wa Natani anayang'anira akapitao, ndipo Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi nduna yopangira mfumu,


Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m'dziko muno pamaso pa ana anu Israele, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha?


Ha? Munthu akadapembedzera mnzake kwa Mulungu, monga munthu apembedzera mnansi wake!


Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m'chihemamo.


Koma iwe, Israele, mtumiki wanga, Yakobo, amene ndinakusankha, mbeu ya Abrahamu bwenzi langa;


Kodi simunawerenge ngakhale lembo ili, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unayesedwa mutu wa pangodya:


Ndipo anapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri; mmodzi kudzanja lake lamanja ndi wina kulamanzere.


Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m'makutu anu.


Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davide za Yudasi, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.


Mulungu sanataye anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kapena simudziwa kodi chimene lembo linena za Eliya? Kuti anaumirira Mulungu poneneza Israele, kuti,


Pakuti lembo linena kwa Farao, Chifukwa cha ichi, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe padziko lonse lapansi.


Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo.


Monga Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kunawerengedwa kwa iye chilungamo,


Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo:


Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha.


Chifukwa kwalembedwa m'lembo, Taona, ndiika mu Ziyoni mwala wotsiriza wa pangodya, wosankhika, wa mtengo wake; ndipo wokhulupirira Iye sadzanyazitsidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa