Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Tito 3:9 - Buku Lopatulika

9 koma pewa mafunso opusa, ndi mawerengedwe a mibadwo, ndi ndeu, ndi makani a pamalamulo; pakuti sizipindulitsa, ndipo zili zachabe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 koma pewa mafunso opusa, ndi mawerengedwe a mibadwo, ndi ndeu, ndi makani a pamalamulo; pakuti sizipindulitsa, ndipo zili zachabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma upewe kufufuzafufuza zopusa, kumaŵerengaŵerenga ndondomeko za maina a makolo, mikangano, ndi mitsutso pa za Malamulo a Mose. Zimenezi nzosathandiza, zilibe phindu konse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Koma upewe kufufuzafufuza zopusa, kuwerengawerenga mndandanda wa mibado ya makolo, mikangano ndi mitsutso pa za Malamulo, chifukwa zimenezi ndi zosapindulitsa ndi zopanda pake.

Onani mutuwo Koperani




Tito 3:9
10 Mawu Ofanana  

Kodi atsutsane ndi mnzake ndi mau akusathandiza? Kapena ndi maneno akusapindulitsa?


Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.


Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: Tidziwa kuti tili nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chitukumula, koma chikondi chimangirira.


koma nkhani zachabe ndi za akazi okalamba ukane. Ndipo udzizoloweretse kuchita chipembedzo;


Uwakumbutse izi, ndi kuwachitira umboni pamaso pa Ambuye, kuti asachite makani ndi mau osapindulitsa kanthu, koma ogwetsa iwo akumva.


Koma pewa nkhani zopanda pake; pakuti adzapitirira kutsata chisapembedzo,


Koma mafunso opusa ndi opanda malango upewe, podziwa kuti abala ndeu.


osasamala nthano zachabe za Chiyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana nacho choonadi.


Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa