Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 4:9 - Buku Lopatulika

9 Nati Bowazi kwa akulu, ndi kwa anthu onse, Inu ndinu mboni lero lino kuti ndagula zonse za Elimeleki, ndi zonse za Kilioni, ndi Maloni, padzanja la Naomi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Nati Bowazi kwa akulu, ndi kwa anthu onse, Inu ndinu mboni lero lino kuti ndagula zonse za Elimeleki, ndi zonse za Kilioni, ndi Maloni, pa dzanja la Naomi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsono Bowazi adauza atsogoleri ndi anthu onse aja kuti, “Nonsenu ndinu mboni lero, kuti ine ndagula kwa Naomi zonse zimene zidaali za malemu Elimeleki, ndiponso zonse za malemu Kiliyoni ndi za malemu Maloni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndipo Bowazi anawuza akuluakuluwo ndi anthu onse aja kuti, “Nonsenu ndinu mboni lero, kuti ine ndagula kwa Naomi zonse zimene zinali za malemu Elimeleki, zonse zimene zinali za malemu Kiliyoni ndiponso za malemu Maloni.

Onani mutuwo Koperani




Rute 4:9
6 Mawu Ofanana  

Iai, mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga lili m'menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu.


Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu ku Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Mowabu, nakhala komweko.


Ndiponso Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa cholowa chake; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ake, ndi pa chipata cha malo ake; inu ndinu mboni lero lino.


Ndipo woombolayo anati kwa Bowazi, Udzigulire wekha kadzikoko. Navula nsapato yake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa