Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 2:9 - Buku Lopatulika

9 Maso ako akhale pamunda achekawo, ndi kuwatsata; kodi sindinawauze anyamata asakukhudze? Ndipo ukamva ludzu, muka kumitsuko, ukamweko otunga anyamatawo,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Maso ako akhale pa munda achekawo, ndi kuwatsata; kodi sindinawauza anyamata asakukhudze? Ndipo ukamva ludzu, muka kumitsuko, ukamweko otunga anyamatawo,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Uziyang'ana munda akukololawu, ndipo uziŵatsata pambuyo. Ndaŵauza anyamatawo kuti asakuvute. Tsono ukamamva ludzu, uzipita ku mitsuko ndi kukamwa madzi amene anyamatawo atunga.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Uziyangʼana munda akukolola anyamatawo akamakolola mʼmundamu, ndipo iwe uzitsata pambuyo pawo. Ndawawuza anyamatawo kuti asakuvutitse. Ndipo ukamva ludzu, uzipita ku mitsuko ndi kukamwa madzi amene anyamatawa atunga.”

Onani mutuwo Koperani




Rute 2:9
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleze iwe kuti umkhudze mkaziyo.


Ndichitireni chifundo, ndichitireni chifundo, mabwenzi anga inu; pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.


Ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga, musamachitira choipa aneneri anga.


Chomwecho wolowa kwa mkazi wa mnzake; womkhudzayo sadzapulumuka chilango.


Ndipo aliyense amene adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.


Koma za izi munalembazi; kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi.


Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.


Potero anagwa nkhope yake pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?


Pamenepo Bowazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakhunkha m'munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa