Obadiya 1:13 - Buku Lopatulika13 Usalowe m'mudzi wa anthu anga tsiku la tsoka lao, kapena kupenyerera iwe choipa chao tsiku la tsoka lao, kapena kuthira manja khamu lao tsiku la tsoka lao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Usalowe m'mudzi wa anthu anga tsiku la tsoka lao, kapena kupenyerera iwe choipa chao tsiku la tsoka lao, kapena kuthira manja khamu lao tsiku la tsoka lao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kuloŵa mu mzinda wa anthu anga. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kuŵanyodola. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kulanda chuma chao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Iwe sunayenera kudutsa pa zipata za anthu anga pa nthawi ya masautso awo, kapena kuwanyogodola pa tsiku la tsoka lawo, kapena kulanda chuma chawo pa nthawi ya masautso awo. Onani mutuwo |