Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 7:84 - Buku Lopatulika

84 Uku ndi kupereka chiperekere guwa la nsembe, ndi akalonga a Israele, tsiku la kudzoza kwake: mbale zasiliva khumi ndi ziwiri, mbale zowazira zasiliva khumi ndi ziwiri, zipande zagolide khumi ndi ziwiri;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

84 Uku ndi kupereka chiperekere guwa la nsembe, ndi akalonga a Israele, tsiku la kudzoza kwake: mbale zasiliva khumi ndi ziwiri, mbale zowazira zasiliva khumi ndi ziwiri, zipande zagolide khumi ndi ziwiri;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

84 Zopereka zopatulira guwa zimene atsogoleri a Aisraele adapereka pa tsiku limene guwalo lidadzozedwa, nazi: adapereka mbale zasiliva khumi ndi ziŵiri, mikhate yasiliva khumi ndi iŵiri, timbale tagolide khumi ndi tiŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

84 Zopereka za atsogoleri a Israeli zopatulira guwa lansembe pamene linadzozedwa zinali izi: mbale khumi ndi ziwiri zasiliva, mabeseni owazira asiliva khumi ndi awiri ndi mbale zagolide khumi ndi ziwiri.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 7:84
11 Mawu Ofanana  

Ndipo uzipanga mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo; uzipanga za golide woona.


Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kuutsa chihema, nachidzoza ndi kuchipatula, ndi zipangizo zake zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;


Ndipo akalonga anabwera nazo za kupereka chiperekere guwa la nsembe tsiku lodzozedwa ili; inde akalongawo anabwera nacho chopereka chao paguwa la nsembelo.


ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ichi ndi chopereka cha Ahira mwana wa Enani.


mbale yasiliva yonse masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, ndi mbale yowazira yonse masekeli makumi asanu ndi awiri; siliva wonse wa zotengerazo ndizo masekeli zikwi ziwiri ndi mazana anai, kuyesa sekeli wa malo opatulika.


Tili nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema alibe ulamuliro wa kudyako.


Ndipo linga la mzinda linakhala nao maziko khumi ndi awiri, ndi pomwepo maina khumi ndi awiri a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa