Numeri 31:47 - Buku Lopatulika47 mwa gawolo la ana a Israele Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201447 mwa gawolo la ana a Israele Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa Kachisi wa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa47 Pa gawo la Aisraelelo, Mose adatengako chofunkha chimodzi pa zofunkha makumi asanu aliwonse, anthu ndi nyama, ndipo adapatsa Alevi amene ankayang'anira Chihema cha Chauta, monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero47 Kuchoka pa gawo la Aisraelilo, Mose anatengapo chimodzi pa zolanda ku nkhondo makumi asanu aliwonse, anthu ndi nyama, ndipo anazipereka kwa Alevi amene ankayangʼanira tenti ya Yehova monga Yehova analamulira Mose. Onani mutuwo |