Numeri 30:14 - Buku Lopatulika14 Koma mwamuna wake akhala naye chete tsiku ndi tsiku; pamenepo akhazikira zowinda zake zonse, kapena zodziletsa zake zonse, zili pa iye; wazikhazikitsa, popeza anakhala naye chete tsikuli anazimva iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Koma mwamuna wake akhala naye chete tsiku ndi tsiku; pamenepo akhazikira zowinda zake zonse, kapena zodziletsa zake zonse, zili pa iye; wazikhazikitsa, popeza anakhala naye chete tsikuli anazimva iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Koma ngati m'maŵa mwake ndi masiku otsatirawo mwamuna wake samkaniza, atamva zimenezo, mkaziyo achitedi zonse zimene adalumbira, kapena zimene adalonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa choti sadamuuze kanthu mkaziyo pa tsiku limene adamva. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Ndipo ngati mmawa mwake ndi masiku otsatira mwamuna wake sanenapo kanthu atamva zimenezi, mayiyo achitedi zimene walumbira kapena zimene walonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa sanamuwuze kanthu mayiyo pa tsiku limene anamva akulonjeza kapena kulumbira. Onani mutuwo |