12 Koma ngati mwamuna wake anazifafanizadi tsiku lakuzimva iye, zonse zotuluka m'milomo yake kunena za zowinda zake, kapena za chodziletsa cha moyo wake sizidzakhazikika; mwamuna wake anafafaniza; ndipo Yehova adzamkhululukira iye.
12 Koma ngati mwamuna wake anazifafanizadi tsiku lakuzimva iye, zonse zotuluka m'milomo yake kunena za zowinda zake, kapena za chodziletsa cha moyo wake sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira iye.
Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.
Ndipo wansembe azichita chotetezera khamu lonse la ana a Israele, ndipo adzakhululukidwa; popeza sanachite dala, ndipo anadza nacho chopereka chao, nsembe yamoto kwa Yehova, ndi nsembe yao yauchimo pamaso pa Yehova, chifukwa cha kulakwa osati dala.
ndipo mwamuna wake anamva, koma anakhala naye chete osamletsa, pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi zodziletsa zonse anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika.
Koma atate wake akamletsa tsiku lakumva iye; zowinda zake zonse, ndi zodziletsa zake zonse anamanga nazo moyo wake, sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira, popeza atate wake anamletsa.
Koma mwamuna wake akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza chowinda chake anali nacho, ndi zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake; ndipo Yehova adzamkhululukira.