Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 29:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo tsiku lachiwiri muzibwera nazo ng'ombe zamphongo khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai a chaka chimodzi, opanda chilema;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo tsiku lachiwiri muzibwera nazo ng'ombe zamphongo khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai a chaka chimodzi, opanda chilema;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 “Pa tsiku lachiŵiri mupereke anaang'ombe khumi ndi aŵiri amphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi opanda chilema,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 “ ‘Pa tsiku lachiwiri muzipereka ana angʼombe aamuna khumi ndi awiri aja, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi aja, zonse zopanda chilema.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 29:17
14 Mawu Ofanana  

Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo; mwanditsegula makutu. Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapemphe.


Ndipo chidzakomera Yehova koposa ng'ombe, inde mphongo za nyanga ndi ziboda.


Mwanawankhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa chaka chimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.


Nditani nazo nsembe zanu zochulukazo? Ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa anaankhosa, ngakhale wa atonde.


Pakuti ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu kuposa nsembe zopsereza.


Masiku asanu ndi awiri mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; tsiku lachisanu ndi chitatu mukhale nao msonkhano wopatulika; ndipo mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; ndilo lotsirizira; musamagwira ntchito ya masiku ena.


ndipo mubwere nayo nsembe yopsereza, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe zamphongo khumi ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, akhale opanda chilema;


Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.


Pakunena Iye, Latsopano, anagugitsa loyambali. Koma chimene chilinkuguga ndi kusukuluka, chayandikira kukanganuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa