Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 29:14 - Buku Lopatulika

14 ndi nsembe yake yaufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a efa wa ng'ombe imodzi, momwemo nazo ng'ombe khumi ndi zitatuzo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, momwemo nazo nkhosa zamphongo ziwirizo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 ndi nsembe yake yaufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a efa wa ng'ombe imodzi, momwemo nazo ng'ombe khumi ndi zitatuzo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, momwemo nazo nkhosa zamphongo ziwirizo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Muperekenso choperaka cha chakudya chosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongo iliyonse,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Pa mwana wangʼombe aliyense mwa ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu aja, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Pa nkhosa iliyonse mwa nkhosa ziwiri zija, mukonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 29:14
3 Mawu Ofanana  

Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge anaankhosa awiri, amuna opanda chilema, ndi mwanawankhosa mmodzi wamkazi wa chaka chimodzi wopanda chilema, ndi atatu a magawo khumi a efa la ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa magawo atatu wa mafuta.


ndipo mubwere nayo nsembe yopsereza, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe zamphongo khumi ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, akhale opanda chilema;


ndi limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo nao anaankhosa khumi ndi anai;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa