Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 28:19 - Buku Lopatulika

19 koma mubwere nayo nsembe yamoto, nsembe yopsereza ya Yehova; ng'ombe ziwiri zamphongo, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 koma mubwere nayo nsembe yamoto, nsembe yopsereza ya Yehova; ng'ombe ziwiri zamphongo, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 koma mupereke nsembe yotentha pa moto, nsembe yopsereza ya Chauta. Ikhale ya anaang'ombe aŵiri amphongo, nkhosa yamphongo imodzi ndi anaankhosa asanu ndi aŵiri a chaka chimodzi, opanda chilema.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Koma muzipereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri aamuna a chaka chimodzi, onsewo wopanda chilema.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 28:19
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anachotsapo nsembe zopsereza, kuti azipereke kwa ana a anthu monga mwa magawidwe a nyumba za makolo; azipereke kwa Yehova monga mulembedwa m'buku la Mose. Natero momwemo ndi ng'ombezo.


Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.


Musamabwera nayo yokhala ndi chilema; popeza siidzalandirikira inu.


ndi nsembe yao ya efa wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; mupereke atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe, ndi awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo;


Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, zikhale kwa inu zopanda chilema, ndi nsembe zake zothira.


koma mubwere nayo nsembe yopsereza kwa Yehova, ya fungo lokoma; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema;


Koma ikakhala nacho chilema, yotsimphina, kapena yakhungu, chilema chilichonse choipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu.


Ndipo muziphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, ya nkhosa ndi ya ng'ombe, m'malo amene Yehova adzasankha kukhalitsamo dzina lake.


koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwanawankhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa