Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 25:15 - Buku Lopatulika

15 Ndi dzina la mkazi Mmidiyani adamuphayo ndiye Kozibi mwana wamkazi wa Zuri; ndiye mkulu wa anthu a nyumba ya makolo mu Midiyani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndi dzina la mkazi Mmidiyani adamuphayo ndiye Kozibi mwana wamkazi wa Zuri; ndiye mkulu wa anthu a nyumba ya makolo m'Midiyani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Ndipo mkazi Wachimidiyani amene adaphedwayo anali Kozibi mwana wa Zuri, amene anali mtsogoleri wa mbumba ina ya fuko la ku Midiyani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Ndipo dzina la mkazi wa Chimidiyani, yemwe anaphedwayo, linali Kozibi mwana wa Zuri, mtsogoleri wa fuko la ku Midiyaniko.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 25:15
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Mowabu anati kwa akulu a Midiyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse zili pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Mowabu masiku amenewo.


Koma dzina la Mwisraele adamuphayo, ndiye amene adamupha pamodzi ndi mkazi Mmidiyani, ndiye Zimiri mwana wa Salu, mfumu ya nyumba ya makolo mwa Asimeoni.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,


popeza akusautsani ndi manyengo ao amene anakunyengani nao; m'chija cha Peori, ndi cha Kozibi, mwana wamkazi wa kalonga wa ku Midiyani, mlongo wao, amene adamupha tsiku la mliri, m'chija cha Peori.


Ndipo anapha mafumu a Amidiyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.


ndi mizinda yonse ya kuchidikha, ndi ufumu wonse wa Sihoni mfumu ya Aamori, wochita ufumu mu Hesiboni, amene Mose anamkantha pamodzi ndi akalonga a Midiyani, Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri ndi Reba, akalonga a Sihoni, nzika za m'dziko.


Koma ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Midiyani zaka zisanu ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa