Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 25:11 - Buku Lopatulika

11 Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israele, popeza anachita nsanje ndi nsanje yanga pakati pao, kotero kuti sindinawathe ana a Israele m'nsanje yanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israele, popeza anachita nsanje ndi nsanje yanga pakati pao, kotero kuti sindinawatha ana a Israele m'nsanje yanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 “Finehasi mwana wa Eleazara, mdzukulu wa Aroni, wandiletsa kuti ndisaŵaononge Aisraele, chifukwa choti sadalole kuti wina aliyense apembedze mulungu wina koma Ine, nchifukwa chake sindidaŵaononge ndili wokwiya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni wabweza mkwiyo wanga pa Aisraeli chifukwa sanalole kuti wina aliyense apembedze mulungu wina koma Ine ndekha. Nʼchifukwa chake sindinawawononge mu mkwiyo wanga.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 25:11
24 Mawu Ofanana  

Naika mafupa a Saulo ndi Yonatani mwana wake ku dziko la Benjamini mu Zela, m'manda a Kisi atate wake; nachita zonse inalamulira mfumu. Ndipo pambuyo pake Mulungu anapembedzeka za dzikolo.


Ndipo Ayuda anachita zoipa pamaso pa Yehova, namchititsa nsanje ndi zoipa zao anazichitazo, zakuposa zija adazichita makolo ao.


Potero Iye adati awaononge, pakadapanda Mose wosankhika wake, kuima pamaso pake pogamukapo, kubweza ukali wake ungawaononge.


Pamenepo panauka Finehasi, nachita chilango: Ndi mliriwo unaletseka.


Ndipo adamuyesa iye wachilungamo, ku mibadwomibadwo kunthawi zonse.


Ndipo anautsa mtima wake ndi malo amsanje ao, namchititsa nsanje ndi mafano osema.


Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;


Munthu akadyetsa choweta pabusa kapena pamunda wampesa, atamasula choweta chake, ndipo chitadya podyetsa pa mwini wake; alipe podyetsa pake poposa, ndi munda wa mphesa wake woposa.


pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje;


Ndipo ndidzaweruza mlandu wako, monga aweruza akazi achigololo ndi okhetsa mwazi; ndipo ndidzakutengera mwazi wa ukali ndi wa nsanje.


Yehova ndiye Mulungu wansanje, nabwezera chilango; Yehova ndiye wobwezera chilango, ndi waukali ndithu; Yehova ndiye wobwezera chilango oyambana naye, nasungira mkwiyo pa adani ake.


Ngakhale siliva wao, ngakhale golide wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko.


Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.


Kapena kodi tichititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa Iye?


Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.


Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo.


Anamchititsa nsanje ndi milungu yachilendo, anautsa mkwiyo wake ndi zonyansa.


Anautsa nsanje yanga ndi chinthu chosati Mulungu; anautsa mkwiyo wanga ndi zopanda pake zao. Ndidzautsa nsanje yao ndi iwo osakhala mtundu wa anthu; ndidzautsa mkwiyo wao ndi mtundu wa anthu opusa.


Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye moto wonyeketsa, ndi Mulungu wansanje.


Ndipo ana a Israele anatumiza kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, Finehasi mwana wa Eleazara wansembe,


Ndipo Yoswa anati kwa anthu, Simungathe inu kutumikira Yehova pakuti ndiye Mulungu woyera, ndi Mulungu wansanje; sadzalekerera zolakwa zanu, kapena zochimwa zanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa