Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 24:6 - Buku Lopatulika

6 Ziyalika monga zigwa, monga minda m'mphepete mwa nyanja, monga khonje wooka Yehova, monga mikungudza m'mphepete mwa madzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ziyalika monga zigwa, monga minda m'mphepete mwa nyanja, monga khonje wooka Yehova, monga mikungudza m'mphepete mwa madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Anthu ako ali ngati zigwa zofika patali, ali ngati minda ya m'mbali mwa mtsinje, ali ngati khonje amene Chauta adabzala, ali ngati mitengo ya mkungudza yomera m'mbali mwa madzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “Monga zigwa zotambalala, monga minda mʼmbali mwa mtsinje, monga aloe wodzalidwa ndi Yehova, monga mikungudza mʼmbali mwa madzi.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 24:6
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.


Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.


Mitengo ya Yehova yadzala ndi madzi; mikungudza ya ku Lebanoni imene anaioka;


Zovala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasiya; m'zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njovu mwatuluka zoimba za zingwe zokukondweretsani.


Ndinatsikira kumunda wa mtedza, kukapenya msipu wa m'chigwa, kukapenya ngati pamipesa paphuka, ngati pamakangaza patuwa maluwa.


Ndidzabzala m'chipululu mkungudza, ndi msangu, ndi kasiya, ndi mtengo wa azitona; ndidzaika m'chipululu pamodzi mlombwa, ndi mkuyu, ndi naphini;


ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse.


Iwo akhale ndi manyazi amene andisautsa ine, koma ine ndisakhale ndi manyazi; aopsedwe iwo, koma ndisaopsedwe ine; muwatengere iwo tsiku la choipa, muwaononge ndi chionongeko chowirikiza.


Ndipo adzadza nadzaimba pa msanje wa Ziyoni, nadzasonkhanira ku zokoma za Yehova, kutirigu, ndi kuvinyo, ndi mafuta, ndi kwa ana a zoweta zazing'ono ndi zazikulu; ndipo moyo wao udzakhala ngati munda wamichera; ndipo sadzakhalanso konse ndi chisoni.


Ndipo kumtsinje, kugombe kwake tsidya lino ndi lija, kudzamera mtengo uliwonse wa chakudya, osafota tsamba lake, zipatso zake zomwe zosasowa; idzabala zipatso zatsopano mwezi ndi mwezi, popeza madzi ake atumphuka m'malo opatulika; ndi zipatso zake zidzakhala chakudya, ndi tsamba lake lakuchiritsa.


Ndipo kudzachitika tsiku ilo mapiri adzakhetsa vinyo wozuna, ndi pazitunda padzayenda mkaka, ndi m'mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi; ndi madzi akasupe adzatuluka m'nyumba ya Yehova, nadzamwetsa madzi chigwa cha Sitimu.


Ha? Mahema ako ngokoma, Yakobo; zokhalamo zako, Israele!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa