Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 23:4 - Buku Lopatulika

4 Pamenepo Mulungu anakomana ndi Balamu; ndipo ananena ndi iye, Ndakonza maguwa a nsembe asanu ndi awiri, ndipo ndapereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo paguwa la nsembe lililonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Pamenepo Mulungu anakomana ndi Balamu; ndipo ananena ndi iye, Ndakonza maguwa a nsembe asanu ndi awiri, ndipo ndapereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe lililonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mulungu adakumana ndi Balamu, ndipo Balamuyo adati, “Ndakonza maguwa asanu ndi aŵiri, ndipo pa guwa lililonse ndaperekapo ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mulungu anakumana naye ndipo Balaamu anati, “Ndakonza maguwa asanu ndi awiri ndipo pa guwa lililonse ndaperekapo nsembe ya ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzinso.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 23:4
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kunka nao, koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukachite.


Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu, nati, Anthu awa ali ndi iwe ndiwo ayani?


Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Ndimangireni kuno maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere kuno ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.


Ndipo Yehova anakomana naye Balamu, naika mau m'kamwa mwake, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene chakutichakuti.


Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Imani pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine, kapena Yehova akadza kukomana ndi ine; ndipo chimene akandionetsa ine ndidzakufotokozerani. Ndipo anapita pamsanje poyera.


Ndipo Yehova anaika mau m'kamwa mwa Balamu, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene chakutichakuti.


nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake.


ndisala chakudya kawiri sabata limodzi; ndipereka limodzi la magawo khumi la zonse ndili nazo.


Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


Pamenepo kudzitama kuli kuti? Kwaletsedwa. Ndi lamulo lotani? La ntchito kodi? Iai; koma ndi lamulo la chikhulupiriro.


chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa