Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 23:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Balaki anachita monga Balamu ananena; ndipo Balaki ndi Balamu anapereka paguwa la nsembe lililonse ng'ombe ndi nkhosa yamphongo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Balaki anachita monga Balamu ananena; ndipo Balaki ndi Balamu anapereka pa guwa la nsembe lililonse ng'ombe ndi nkhosa yamphongo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Balaki adachitadi monga momwe adamuuzira Balamu. Ndipo Balaki pamodzi ndi Balamu adapereka ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo pa guwa lililonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo awiriwo anapereka ngʼombe imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 23:2
6 Mawu Ofanana  

Ndipo masiku asanu ndi awiri a chikondwerero akonzere Yehova nsembe yopsereza, ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri zopanda chilema, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiriwa; ndi tonde tsiku ndi tsiku, akhale wa nsembe yauchimo.


Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Ndimangireni kuno maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere kuno ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.


Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo paguwa la nsembe lililonse.


Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Mundimangire pano maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere pano ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.


Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Imani pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine, kapena Yehova akadza kukomana ndi ine; ndipo chimene akandionetsa ine ndidzakufotokozerani. Ndipo anapita pamsanje poyera.


Ndipo Balaki anachita monga adanena Balamu, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo paguwa la nsembe lililonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa