Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 22:29 - Buku Lopatulika

29 Pamenepo Balamu anati kwa bulu, Chifukwa wandipeputsa; mukadakhala lupanga m'dzanja langa tsopano, ndikadakupha iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Pamenepo Balamu anati kwa bulu, Chifukwa wandipeputsa; mukadakhala lupanga m'dzanja langa tsopano, ndikadakupha iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Balamu adauza buluyo kuti, “Chifukwa choti ukuseŵera nane, ndikadakhala ndi lupanga m'manja mwanga, ndikadakupha.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Balaamu anati kwa buluyo, “Wandipusitsa, ndikanakhala ndi lupanga mʼmanja mwanga, ndikanakupha pomwe pano.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 22:29
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Labani anati, Taona, kukhale monga mau ako.


Wolungama asamalira moyo wa choweta chake; koma chifundo cha oipa ndi nkhanza.


Mkwiyo wa chitsiru udziwika posachedwa; koma wanzeru amabisa manyazi.


Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.


Ndipo bulu anati kwa Balamu, Si ndine bulu wako amene umayenda wokwera pa ine chiyambire ndili wako kufikira lero lino? Kodi ndikakuchitira chotere ndi kale lonse? Ndipo anati, Iai.


Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa