Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 22:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Koma Balamu adayankha atumiki a Balakiwo kuti, “Ngakhale Balaki akadati andipatse nyumba yake yodzaza ndi siliva ndi golide, sindikadatha kuchita zosiyana ndi zimene Chauta, Mulungu wanga, wandilamula. Sindikadatha kuchepetsa kapena kuwonjeza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Koma Balaamu anayankha atumiki a Balaki kuti, “Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingachite chilichonse chachikulu kapena chachingʼono kuposa kuchita lamulo la Yehova Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 22:18
14 Mawu Ofanana  

Ndipo munthu wa Mulungu ananena ndi mfumu, Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowe kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno.


Koma Mikaya anati, Pali Yehova, zimene Yehova adzanena nane ndidzanena ine.


Nati Mikaya, Pali Yehova, chonena Mulungu wanga ndidzanena chomwechi.


kapena pamodzi ndi akalonga eni ake a golide, odzaza nyumba zao ndi siliva;


Pamenepo anayankha Daniele, nati kwa mfumu, Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphotho zanu mupatse wina; koma ndidzawerengera mfumu lembalo, ndi kumdziwitsa kumasulira kwake.


Ndikupemphani, tsono, khalani pano inu usiku uno womwe; kuti ndidziwe chomwe Yehova adzanenanso nane.


Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Taonani, ndafika kwa inu; ngati ndili nayo mphamvu konse tsopano kunena kanthu? Mau amene Mulungu aike m'kamwa mwanga ndiwo ndidzanena.


Ndipo ananena nao, Mugone kuno usiku uno, ndidzakubwezerani mau, monga Yehova adzanena ndi ine; pamenepo mafumu a Mowabu anagona ndi Balamu.


Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Chilichonse achinena Yehova, chomwecho ndizichita?


Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Kodi sindinauzanso amithenga anu amene munawatumiza kwa ine, ndi kuti,


Chinkana Balaki akandipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kuchita chokoma kapena choipa ine mwini wake; chonena Yehova ndicho ndidzanena ine?


Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama.


Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.


koma sindinafuna kumvera Balamu, potero anakudalitsani chidalitsire, ndipo ndinakulanditsani m'dzanja lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa