Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 2:25 - Buku Lopatulika

25 Mbendera ya chigono cha Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezere mwana wa Amisadai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Mbendera ya chigono cha Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezere mwana wa Amisadai.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 “Mbali yakumpoto kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Dani, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Danilo ndi Ahiyezere mwana wa Amishadai,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Kumpoto kudzakhala msasa wa magulu a Dani pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Adani ndi Ahiyezeri mwana wa Amisadai.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 2:25
7 Mawu Ofanana  

Wa Dani, Ahiyezere mwana wa Amisadai.


A ana a Dani, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;


Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Ahiyezere mwana wa Amisadai.


Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.


Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja la Merari ndiye Zuriyele mwana wa Abihaili; azimanga mahema ao pa mbali ya chihema cha kumpoto.


Tsiku lakhumi kalonga wa ana a Dani, ndiye Ahiyezere mwana wa Amisadai:


ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Ahiyezere mwana wa Amisadai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa