Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 19:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo iye wakutentha ng'ombeyo atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo iye wakutentha ng'ombeyo atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Munthu amene atentha ng'ombeyo achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma adzakhalebe woipitsidwa mpaka madzulo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Munthu amene amawotcha ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake ndi kusamba ndi madzi. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 19:8
6 Mawu Ofanana  

ndipo aliyense akanyamulako nyama ya mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndi iye amene anazitentha atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, ndipo atatero alowenso kuchigono.


Ndipo aliyense wakudya yakufa yokha, kapena yojiwa kuthengo, ngakhale ndiye wa m'dziko kapena mlendo, azitsuka nsalu zake, nasambe ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo adzakhala woyera.


Ndipo likhale kwa iwo lemba losatha; kuti iye wakuwaza madzi akusiyanitsa azitsuka zovala zake; ndi iye wakukhudza madzi akusiyanitsa adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Pamenepo wansembe atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi; ndipo atatero alowenso kuchigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo munthu woyera aole mapulusa a ng'ombe yaikaziyo, nawaike kunja kwa chigono, m'malo moyera: ndipo awasungire khamu la ana a Israele akhale a madzi akusiyanitsa; ndiwo nsembe yauchimo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa