Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 18:32 - Buku Lopatulika

32 Ndipo simudzasenzapo uchimo, mutakwezako zokometsetsa zake; ndipo musamaipsa zinthu zopatulika za ana a Israele, kuti mungafe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndipo simudzasenzapo uchimo, mutakwezako zokometsetsa zake; ndipo musamaipsa zinthu zopatulika za ana a Israele, kuti mungafe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Ndipo simudzachimwa mukadya zimenezo, ngati mwapereka kale kwa Chauta zabwino kopambana zina zonse. Motero simudzanyoza zinthu zoyera za Aisraele ndipo simudzafa.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Popereka gawo labwino kwambirilo simudzapezeka olakwa. Mukatero simudzadetsa zopereka zoyera za Aisraeli, ndipo simudzafa.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 18:32
10 Mawu Ofanana  

Ndipo azivale Aroni ndi ana ake, pakulowa iwo ku chihema chokomanako, kapena poyandikiza iwo kuguwa la nsembe kutumikira m'malo opatulika; anganyamule mphulupulu, nangafe; likhale lemba losatha la iye ndi mbumba zake pambuyo pake.


koma aliyense akudyako adzasenza mphulupulu yake, popeza waipsa chopatulidwa cha Yehova; ndi munthuyu amsadze, kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.


Nena ndi Aroni ndi ana ake aamuna, kuti azikhala padera ndi zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene amandipatulira Ine, ndipo asaipse dzina langa loyera; Ine ndine Yehova.


Mupereka mkate wodetsedwa paguwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M'menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka.


Ndipo kuyambira tsopano ana a Israele asayandikize chihema chokomanako, angamasenze uchimo kuti angafe.


Ndipo muzidye pamalo ponse, inu ndi a pabanja panu; popeza ndizo mphotho yanu mwa ntchito yanu m'chihema chokomanako.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,


Chifukwa chake yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.


Pakuti iye wakudya ndi wakumwa, adya namwa chiweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupilo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa