Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 18:30 - Buku Lopatulika

30 Chifukwa chake unene nao, Pamene mukwezako zokometsetsa zake, zidzayesedwanso kwa Alevi ngati zipatso za padwale, ndi zipatso za mopondera mphesa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Chifukwa chake unene nao, Pamene mukwezako zokometsetsa zake, zidzayesedwanso kwa Alevi ngati zipatso za padwale, ndi zipatso za mopondera mphesa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Nchifukwa chake uŵauze kuti, ‘Mutaperekako zabwino kopambana zina zonse, zotsalazo muziŵerengere kuti nzanu, monga tirigu woyamba kucha amene anthu amapuntha, ndiponso mphesa zoyamba kucha zimene amapsinya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 “Nena kwa Alevi: ‘Pamene mupereka gawo labwino lopambana zonse, gawo limenelo lidzawerengedwa kwa inu ngati lochokera popunthira tirigu kapenanso kopsinyira mphesa.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 18:30
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Israele atate wao anati kwa iwo, Ngati chomwecho tsopano chitani ichi: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta amankhwala pang'ono, ndi uchi pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;


Ndipo anafika pa dwale la Atadi, lili tsidya lija la Yordani, pamenepo anamlira maliro a atate wake masiku asanu ndi limodzi.


Ndipo upatule nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wam'mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; zili za Aroni, ndi za ana ake aamuna;


Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? Ati Yehova wa makamu.


Mupereke nsembe zokweza zonse za Yehova kuzitenga ku mphatso zanu zonse, kusankhako zokometsetsa ndizo zopatulika zake.


Ndipo muzidye pamalo ponse, inu ndi a pabanja panu; popeza ndizo mphotho yanu mwa ntchito yanu m'chihema chokomanako.


Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.


ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa