Numeri 11:26 - Buku Lopatulika26 Koma amuna awiri anatsalira m'chigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzake ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanatuluke kunka kuchihema; ndipo ananenera m'chigono. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201426 Koma amuna awiri anatsalira m'chigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzake ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanatuluke kunka kuchihema; ndipo ananenera m'chigono. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa26 Anthu aŵiri adatsalira m'mahema, wina anali Elidadi, wina Meladi, ndipo mzimu udakhala pa iwowo. Anali nao m'gulu la olembedwa aja, koma sadapite nao ku chihema chamsonkhano, motero ankalosera m'mahema. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero26 Koma anthu ena awiri omwe mayina awo anali Elidadi ndi Medadi, anatsalira mu msasa. Anali nawo mʼgulu la olembedwa aja, koma sanapite nawo ku Chihema. Komabe mzimu unakhala pa iwo ndipo ananenera ali mu msasa. Onani mutuwo |