Numeri 11:18 - Buku Lopatulika18 Ndipo unene ndi anthu, Mudzipatuliretu, mawa mudzadya nyama; popeza mwalira m'makutu a Yehova, ndi kuti, Adzatipatsa nyama ndani? Popeza tinakhala bwino mu Ejipito. Potero Yehova adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ndipo unene ndi anthu, Mudzipatuliretu, mawa mudzadya nyama; popeza mwalira m'makutu a Yehova, ndi kuti, Adzatipatsa nyama ndani? Popeza tinakhala bwino m'Ejipito. Potero Yehova adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Uŵauze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera zamaŵa, ndipo mudzadya nyama. Inuyo mudalira Chauta alikumva, pamene munkati, “Ndani atipatse nyama tidye? Paja zinthu zinkatiyendera bwino ku Ejipito.” Nchifukwa chake Chauta adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 “Uwawuze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera mawa, pamene mudzadya nyama.’ Yehova anakumvani pamene munkalira kuti, ‘Zikanakhala bwino tikanapeza nyama yoti tidye! Tinkakhala bwino ku Igupto!’ Tsopano Yehova adzakupatsani nyama ndipo mudzayidyadi. Onani mutuwo |