Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 8:17 - Buku Lopatulika

17 Ndi msonkhano wonse wa iwo otuluka m'ndende anamanga misasa, nakhala m'misasamo; pakuti chiyambire masiku a Yoswa mwana wa Nuni kufikira tsiku lija ana a Israele sanatero. Ndipo panali chimwemwe chachikulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndi msonkhano wonse wa iwo otuluka m'ndende anamanga misasa, nakhala m'misasamo; pakuti chiyambire masiku a Yoswa mwana wa Nuni kufikira tsiku lija ana a Israele sanatero. Ndipo panali chimwemwe chachikulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Motero onse amene adaasonkhana, ndiye kuti amene adaabwerako ku ukapolo, adamanga misasa, ndipo adakhala m'menemo. Kuyambira nthaŵi ya Yoswa, mwana wa Nuni, mpaka tsiku limenelo, Aisraele anali asanachitepo zoterozo. Motero kunali chikondwerero chachikulu kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Gulu lonse la anthu limene linabwera ku ukapolo linamanga misasa ndipo linakhala mʼmenemo. Kuyambira nthawi ya Yoswa mwana wa Nuni mpaka tsiku limenelo nʼkuti Aisraeli asanachitepo zimenezi. Choncho panali chimwemwe chachikulu.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 8:17
13 Mawu Ofanana  

nadya namwa pamaso pa Mulungu tsiku lomwelo ndi chimwemwe chachikulu. Ndipo analonga ufumu Solomoni mwana wa Davide kachiwiri, namdzozera Yehova akhale kalonga, ndi Zadoki akhale wansembe.


Momwemo munali chimwemwe chachikulu mu Yerusalemu; pakuti kuyambira masiku a Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele simunachitike chotero mu Yerusalemu.


Panalibe Paska wochitika mu Israele wonga ameneyu, kuyambira masiku a Samuele mneneri; panalibenso wina wa mafumu a Israele anachita Paska wotere, ngati ameneyu anachita Yosiya, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi Ayuda onse, ndi Aisraele opezekako, ndi okhala mu Yerusalemu.


monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika, katatu m'chaka: pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, ndi pa chikondwerero cha Masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa.


Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Masiku asanu ndi awiri muchitire Yehova Mulungu wanu madyerero m'malo amene Yehova adzasankha; popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zipatso zanu zonse, ndi m'ntchito zonse za manja anu; nimukondwere monsemo.


Iwo onse adamwalira m'chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.


Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;


Pakuti ngati Yoswa akadawapumitsa iwo, sakadalankhula m'tsogolomo za tsiku lina.


Ndipo atafa Mose mtumiki wa Yehova, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mnyamata wa Mose,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa