Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 8:16 - Buku Lopatulika

16 Natuluka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yake, ndi m'mabwalo ao, ndi m'mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la Chipata cha Madzi, ndi pa khwalala la Chipata cha Efuremu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Natuluka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yake, ndi m'mabwalo ao, ndi m'mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la Chipata cha Madzi, ndi pa khwalala la chipata cha Efuremu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Choncho anthuwo adapita nakatenga zonsezo ndipo aliyense adadzimangira misasa padenga pa nyumba yake, ndiponso m'mabwalo ao, m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu, m'bwalo la pa Chipata cha Madzi ndi m'bwalo la pa Chipata cha Efuremu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Choncho anthu anapita kukatenga nthambi ndipo aliyense anadzimangira misasa pa denga ya nyumba yake, mʼmabwalo awo, mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, mʼbwalo la pa Chipata cha Madzi ndiponso mʼbwalo la pa Chipata cha Efereimu.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 8:16
12 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.


Ndipo Yehowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Ahaziya, ku Betesemesi, nadza ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira Chipata cha Efuremu kufikira Chipata cha Kungodya, mikono mazana anai.


Ndipo Yehosafati anaima mu msonkhano wa Ayuda, ndi a ku Yerusalemu, kunyumba ya Yehova, pakati pa bwalo latsopano;


Namangiranso khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.


ndi ku Chipata cha ku Chitsime, ndi kundunji kwao, anakwerera pa makwerero a mzinda wa Davide, potundumuka linga, popitirira pa nyumba ya Davide, mpaka ku Chipata cha Madzi kum'mawa.


ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata cha Nsomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka ku Chipata cha Nkhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi.


Koma antchito a m'kachisi okhala mu Ofele anakonza kufikira kumalo a pandunji pa Chipata cha Madzi kum'mawa, ndi nsanja yosomphokayo.


Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi kukhwalala lili ku Chipata cha Madzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la chilamulo cha Mose, chimene Yehova adalamulira Israele.


Nawerenga m'menemo pa khwalala lili ku Chipata cha Madzi kuyambira mbandakucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo.


ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu ina nsembe zothira.


ndipo Ababiloni, olimbana ndi mzinda uwu, adzafika nadzayatsa mzindawu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.


Pamene mumanga nyumba yatsopano, muzimanga kampanda pa tsindwi lake, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa