Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 8:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo m'mawa mwake akulu a nyumba za makolo a anthu onse, ansembe, ndi Alevi anasonkhana pamodzi kwa Ezara mlembi, kuti atole nzeru za mau a chilamulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo m'mawa mwake akulu a nyumba za makolo a anthu onse, ansembe, ndi Alevi anasonkhana pamodzi kwa Ezara mlembi, kuti atole nzeru za mau a chilamulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Atsogoleri a mabanja, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, onse adabwera m'maŵa mwake kwa Ezara, mphunzitsi wa malamulo, kuti aphunzire mau a Malamulowo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Mmawa mwake atsogoleri a mabanja pamodzi ndi ansembe ndi alevi anasonkhana kwa Ezara, mlembi wa malamulo kuti aphunzire mawu a malamulowo.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 8:13
13 Mawu Ofanana  

Ndipo msonkhano wonse unapangana kuchita masiku asanu ndi awiri ena, nachita masiku asanu ndi ena ndi chimwemwe.


Napita anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukulu; popeza anazindikira mau amene adawafotokozera.


Napeza munalembedwa m'chilamulo kuti Yehova analamulira ndi Mose, kuti ana a Israele azikhala m'misasa pa chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri,


Wokonda mwambo akonda kudziwa; koma wakuda chidzudzulo apulukira.


Ndipo anati wina kwa mnzake, Mtima wathu sunali wotentha m'kati mwathu nanga m'mene analankhula nafe m'njira, m'mene anatitsegulira malembo?


Ndipo pakutuluka iwo anapempha kuti alankhule naonso mau awa Sabata likudzalo.


Koma m'mene analikulankhula ndi anthu, ansembe ndi mdindo wa ku Kachisi ndi Asaduki anadzako,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa