Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 6:18 - Buku Lopatulika

18 Pakuti ambiri mu Yuda analumbirirana naye chibwenzi; popeza ndiye mkamwini wake wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wake Yehohanani adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pakuti ambiri m'Yuda analumbirirana naye chibwenzi; popeza ndiye mkamwini wake wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wake Yehohanani adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 pakuti anthu ambiri ku Yuda adaalumbira kuti adzagwirizana naye, chifukwa chakuti anali mkamwini wa Myuda mnzao, Sekaniya, mwana wa Ara. Ndipo mwana wake, Yehohanani, anali atakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu, mwana wa Berekiya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 pakuti anthu ambiri a ku Yuda anali atalumbira kale kuti adzagwira naye ntchito popeza anali mkamwini wa Sekaniya mwana wa Ara, ndipo mwana wake Yehohanani anakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 6:18
7 Mawu Ofanana  

Ndi ana a Hananiya: Pelatiya, ndi Yesaya, ana a Refaya, ana a Arinani, ana a Obadiya, ana a Sekaniya.


Ana a Ara, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu.


Potsatizana naye Hananiya mwana wa Selemiya, ndi Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi, anakonza gawo lina. Potsatizana naye anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya pandunji pa chipinda chake.


Ndi pambali pao anakonza Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi. Ndi pambali pao anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele. Ndi pambali pao anakonza Zadoki mwana wa Baana.


Masikuwo aufulu a Yuda analemberanso makalata ambiri kwa Tobiya; ndipo anawafikanso makalata ake a Tobiya.


Anatchulanso ntchito zake zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza makalata kuti andiopse ine.


Ana a Ara, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa