Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 4:11 - Buku Lopatulika

11 Nati adani athu, Sadzadziwa kapena kuona mpaka talowa pakati pao, ndi kuwapha, ndi kuleketsa ntchitoyi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Nati adani athu, Sadzadziwa kapena kuona mpaka talowa pakati pao, ndi kuwapha, ndi kuleketsa ntchitoyi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Adani athu ankanena zakuti ife Ayuda sitidzadziŵa kapena kuwona kanthu, mpaka iwo atafika pakati pathu, natipha ndi kuletsa ntchito yathuyi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Adani athunso anati, “Iwo asanadziwe izi, kapena kutiona, tidzakhala tili pakati pawo ndipo tidzawapha ndi kuyimitsa ntchitoyo.”

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 4:11
10 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzamgwera ali wolema ndi wofooka, ndi kumuopsa; ndi anthu onse amene ali naye adzathawa; pamenepo ndidzakantha mfumu yokha;


Ndipo Ayuda anati, Mphamvu ya osenza akatundu yatha, ndi dothi lichuluka, motero sitidzakhoza kumanga lingali.


Ndipo kunali, atafika Ayuda okhala pafupi pao ochokera pamalo ponse, anatiuza ife kakhumi, Bwererani kwa ife.


Koma tinapemphera kwa Mulungu wathu, ndi kuwaikira olindirira usana ndi usiku, chifukwa cha iwowa.


Amemezana, alalira, atchereza mapazi anga, popeza alindira moyo wanga.


Chifukwa chake choipa chidzafika pa iwe; sudzadziwa kucha kwake, ndipo chionongeko chidzakugwera; sudzatha kuchikankhira kumbali; ndipo chipasuko chosachidziwa iwe chidzakugwera mwadzidzidzi.


Ndipo kutacha, Ayuda anapangana chiwembu, nadzitemberera, ndi kunena kuti sadzadya kapena kumwa kanthu, kufikira atamupha Paulo;


Pamenepo musakopedwe nao; pakuti amlalira iye oposa makumi anai a iwo amene anadzitemberera okha kuti sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekeratu tsopano nayang'anira lonjezano lanu.


Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa