Nehemiya 13:10 - Buku Lopatulika10 Ndinazindikiranso kuti sanapereke kwa Alevi magawo ao; m'mwemo Alevi ndi oimbira adathawira yense kumunda wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndinazindikiranso kuti sanapereke kwa Alevi magawo ao; m'mwemo Alevi ndi oimbira adathawira yense kumunda wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Ndidapezanso kuti Alevi sankaŵapatsa magawo ao amene ankayenera kulandira. Choncho Aleviwo, pamodzi ndi anthu oimba nyimbo amene ankagwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu, adathaŵa, aliyense kupita ku munda wake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Ndinapezanso kuti Alevi sankalandira magawo awo amene amayera kulandira. Chotsatira chake Alevi onse pamodzi ndi oyimba nyimbo amene ankagwira ku Nyumba ya Mulungu anathawa, aliyense kupita ku munda wake. Onani mutuwo |
ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uliwonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, kuzipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzilimodzi la magawo khumi m'midzi yonse yolima ife.