Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 10:32 - Buku Lopatulika

32 Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka chaka ndi chaka limodzi la magawo atatu a sekeli kuntchito ya nyumba ya Mulungu wathu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka chaka ndi chaka limodzi la magawo atatu a sekeli kuntchito ya nyumba ya Mulungu wathu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Tikulumbiranso kuti chaka ndi chaka tizipereka magaramu anai a siliva, kuti tithandize pa ntchito za ku Nyumba ya Mulungu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 “Tikulonjezanso molumbira kuti chaka ndi chaka tizipereka magalamu anayi a siliva kuti zithandize ntchito ya ku Nyumba ya Mulungu wathu.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 10:32
12 Mawu Ofanana  

ndi mwala umenewu ndinauimiritsa, udzakhala nyumba ya Mulungu; ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani Inu limodzi la magawo khumi.


Kutenga pa zofunkha kunkhondo, anapatulako kukonzera nyumba ya Yehova.


Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m'choponderamo tsiku la Sabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa abulu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza zilizonse, zimene analowa nazo mu Yerusalemu tsiku la Sabata, ndipo ndinawachitira umboni wakuwatsutsa tsikuli anagulitsa zakudya.


Sanatero kodi makolo anu, ndipo Mulungu wathu anatifikitsira ife ndi mzinda uno choipa ichi chonse? Koma inu muonjezera Israele mkwiyo pakuipsa Sabata.


Koma ndinawachitira umboni wakuwatsutsa, ndinanena nao, Mugoneranji pafupi pa linga? Mukateronso ndikuthirani manja. Kuyambira pomwepo sanafikenso pa Sabata.


Kodi ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, tiwakongoletsa ndalama ndi tirigu mwa phindu? Ndikupemphani, tileke phindu ili.


ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;


koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako wa azitona.


Lemekeza Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha;


Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa