Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 8:16 - Buku Lopatulika

16 Pompo ndinapereka mtima wanga kudziwa nzeru, ndi kupenya ntchito zichitidwa pansi pano; kuti anthu saona tulo konse ndi maso ao ngakhale usana ngakhale usiku;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pompo ndinapereka mtima wanga kudziwa nzeru, ndi kupenya ntchito zichitidwa pansi pano; kuti anthu saona tulo konse ndi maso ao ngakhale usana ngakhale usiku;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Ndinkaikapo mtima kuti ndidziŵe nzeru ndi kumvetsa ntchito zimene zikuchitika pansi pano, osapeza tulo usana ndi usiku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Pamene ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe nzeru ndi kuonetsetsa ntchito za munthu pa dziko lapansi, osapeza tulo usana ndi usiku,

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 8:16
11 Mawu Ofanana  

Chotero ndinakhala; usana ludzu linakomola ine, usiku chisanu; tulo tanga tinachoka m'maso mwanga.


Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.


Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimachitidwa pansi pa thambo; ntchito yovuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.


Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima.


Pakuti masiku ake onse ndi zisoni, vuto lake ndi kumliritsa; ngakhale usiku mtima wake supuma. Ichinso ndi chabe.


Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.


Tulo ta munthu wogwira ntchito ntabwino, ngakhale adya pang'ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.


Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;


pakuti sadziwa chimene chidzakhala; pakuti ndani angamuuze nthawi yakuti chidzachitidwa?


Zonsezi ndaziona ndi kuyang'anitsa mtima wanga ntchito zonse zichitidwa pansi pano; nthawi yakuti wina apweteka mnzake pomlamulira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa