Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 5:16 - Buku Lopatulika

16 Ichinso ndi choipa chowawa, chakuti adzangopita monse monga anadza; ndipo wodzisautsa chabe adzaona phindu lanji?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ichinso ndi choipa chowawa, chakuti adzangopita monse monga anadza; ndipo wodzisautsa chabe adzaona phindu lanji?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Chimenechinso nchoipa chomvetsa chisoni kwambiri: kuti munthu adzapita monga momwe adabwerera. Nanga phindu lake nchiyani, popeza kuti iyeyo adagwira pachabe ntchito yolemetsa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Izinso ndi zoyipa kwambiri: munthu adzapita monga momwe anabwerera, ndipo iye amapindula chiyani, pakuti amagwira ntchito yolemetsa yopanda phindu?

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 5:16
13 Mawu Ofanana  

Wovuta banja lake adzalowa m'zomsautsa; wopusa adzatumikira wanzeru.


Kodi ntchito zake zonse munthu asauka nazo zimpindulira chiyani?


Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.


Wogwira Ntchito aona phindu lanji m'chomsautsacho?


Pali choipa chovuta ndachiona kunja kuno, ndicho, chuma chilikupweteka eni ake pochikundika;


Ife tinali ndi pakati, ife tinamva zopweteka, tafanana ngati tabala mphepo; sitinachite chipulumutso chilichonse padziko lapansi; ngakhale okhala m'dziko lapansi sanagwe.


Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? Ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula.


Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kamvulumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzatulutsa ufa; chinkana iutulutsa, alendo adzaumeza.


Pakuti munthu apindulanji akadzilemezera dziko lonse, natayapo moyo wake?


Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.


kuti inunso muvomere otere, ndi yense wakuchita nao, ndi kugwiritsa ntchito.


musapatukire inu kutsata zinthu zachabe, zosapindulitsa, zosapulumutsa, popeza zili zopanda pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa