Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 2:22 - Buku Lopatulika

22 Pakuti munthu ali ndi chiyani m'ntchito zake zonse, ndi m'kusauka kwa mtima wake amasauka nazozo kunja kuno?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Pakuti munthu ali ndi chiyani m'ntchito zake zonse, ndi m'kusauka kwa mtima wake amasauka nazozo kunja kuno?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhaŵa zimene amazichita pansi pano?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhawa zimene amazichita pansi pano?

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 2:22
21 Mawu Ofanana  

Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.


Wantchito adzigwirira yekha ntchito; pakuti m'kamwa mwake mumfulumiza.


Kodi ntchito zake zonse munthu asauka nazo zimpindulira chiyani?


Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.


Wogwira Ntchito aona phindu lanji m'chomsautsacho?


Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja awiri oti thoo pali vuto ndi kungosautsa mtima.


Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.


Inde masiku ake onse amadya mumdima, ndipo zimchulukira chisoni ndi nthenda ndi mkwiyo.


Pompo ndinatama kusekaseka, pakuti munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m'vuto lake masiku onse a moyo wake umene Mulungu wampatsa pansi pano.


Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?


Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.


Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?


Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.


Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala.


Ndipo inu musafunefune chimene mudzadya, ndi chimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima.


kuti inunso muvomere otere, ndi yense wakuchita nao, ndi kugwiritsa ntchito.


Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.


koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimene zitikwanire.


ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa