Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 2:13 - Buku Lopatulika

13 Pamenepo ndinazindikira kuti nzeru ipambana utsiru kwambiri, monga kuunika kupambana mdima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Pamenepo ndinazindikira kuti nzeru ipambana utsiru kwambiri, monga kuunika kupambana mdima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Ndidaona kuti inde nzeru nzopambana uchitsiru, monga momwe kuŵala kumapambanira mdima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndinaona kuti nzeru ndi yopambana uchitsiru, monga momwe kuwala kumapambanira mdima.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 2:13
17 Mawu Ofanana  

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.


Potsegulira mau anu paunikira; kuzindikiritsa opusa.


Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake; koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo.


Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?


Chitsulo chikakhala chosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pochenjeza.


Indetu kuunika nkokoma, maso napeza bwino m'kuona dzuwa.


Nzeru ilimbitsa wanzeru koposa akulu khumi akulamulira m'mzinda.


Pamenepo ndinati, Nzeru ipambana mphamvu; koma anyoza nzeru ya wosauka, osamvera mau ake.


Nzeru ipambana zida za nkhondo; koma wochimwa mmodzi aononga zabwino zambiri.


Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.


Koma ngati diso lako lili loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa. Chifukwa chake ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo ndi waukulu ndithu!


pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa