Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 9:18 - Buku Lopatulika

18 M'mene Iye analikulankhula nao zinthu zimenezo, onani, anadza munthu mkulu, namgwadira Iye, nanena, Wamwalira tsopanoli mwana wanga wamkazi, komatu mudze muike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 M'mene Iye analikulankhula nao zinthu zimenezo, onani, anadza munthu mkulu, namgwadira Iye, nanena, Wamwalira tsopanoli mwana wanga wamkazi, komatu mudze muike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Pamene Yesu ankakamba zimenezi, munthu wina wamkulu adadzamgwadira nati, “Mwana wanga wamkazi wamwalira tsopano apa. Chonde bwerani mudzamsanjike manja, kuti akhale ndi moyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Pamene ankanena zimenezi, mkulu wa sunagoge anabwera namugwadira Iye nati, “Mwana wanga wamkazi wamwalira posachedwapa koma tiyeni mukasanjike dzanja lanu pa iye ndipo adzakhala ndi moyo.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 9:18
25 Mawu Ofanana  

Koma Naamani adapsa mtima, nachoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kutuluka adzanditulukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wake, ndi kuweyula dzanja lake pamalopo, ndi kuchiritsa wakhateyo.


Ndipo iwo amene anali m'ngalawamo anamgwadira, nanena, Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu.


Koma iye anadza, namgwadira Iye, nanena, Ambuye, ndithangateni ine.


Ndipo pamene iwo anadza kukhamu la anthu, kunafika kwa Iye munthu, namgwadira Iye, nati,


Pomwepo anadza kwa Iye amake a ana a Zebedeo ndi ana ake omwe, namgwadira, ndi kumpempha kanthu.


Ndipo pamene anamuona Iye, anamlambira; koma ena anakayika.


Ndipo onani, wakhate anadza namgwadira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza.


Ndipo iwo anadza, namuutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tilikutayika.


Kapena samathira vinyo watsopano m'matumba akale; akatero, matumba aphulika, ndi vinyo atayika, ndi matumba aonongeka; koma athira vinyo watsopano m'matumba atsopano, ndi zonse ziwiri zisungika.


Ndipo Yesu ananyamuka namtsata iye, ndi ophunzira ake omwe.


ananena, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafe koma kali m'tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete.


Ndipo mkulu wa sunagoge anavutika mtima, chifukwa Yesu anachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m'menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.


Ndipo mkulu wina anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi wabwino, ndizichita chiyani, kuti ndilowe moyo wosatha?


Ndipo kapolo wa kenturiyo, wokondedwa naye, anadwala, nafuna kutsirizika.


Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;


Pomwepo Maria, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.


Ndipo m'mene adatha kuwerenga chilamulo ndi aneneri, akulu a sunagoge anatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nao mau akudandaulira anthu, nenani.


Ndipo kunatero kuti atate wake wa Publioyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namchiritsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa