Mateyu 8:33 - Buku Lopatulika33 Koma akuziweta anathawa, namuka kumzinda, nauza zonse, ndi zakuti zao za aziwanda aja. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201433 Koma akuziweta anathawa, namuka kumidzi, nauza zonse, ndi zakuti zao za aziwanda aja. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa33 Oŵeta nkhumbazo adathaŵa. Atakaloŵa mu mzinda, adakasimbira anthu zonse zimene zidachitika, ndiponso zimene zidaŵaonekera ogwidwa ndi mizimu yoipa aja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero33 Koma amene amaziweta anathawa nalowa mʼmudzi nafotokoza zonse, kuphatikizapo zimene zinachitika ndi anthu ogwidwa ndi ziwanda aja. Onani mutuwo |