Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 5:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losamuka thupi lako lonse ku Gehena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losamuka thupi lako lonse ku Gehena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, lidule nkulitaya. Ndi bwino kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kupambana kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 5:30
19 Mawu Ofanana  

Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.


ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo chifukwa cha mau, iye akhumudwa pomwepo.


Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.


Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi Ine.


Ndipo ngati dzanja lako, kapena phazi lako likukhumudwitsa iwe, ulidule, nulitaye; nkwabwino, kuti ulowe m'moyo wopunduka dzanja kapena phazi, koposa kuponyedwa m'moto wa nthawi zonse, uli ndi manja awiri kapena mapazi awiri.


Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye kumdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.


Ndipo uyo amene adalandira matalente asanu anadza, ali nawo matalente ena asanu, nanena, Mbuye, munandipatsa matalente asanu, onani ndapindulapo matalente ena asanu.


Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndipo zidzabalalika nkhosa za gulu.


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.


Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse mu Gehena.


Ndipo ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: nkwabwino kwa iwe kulowa m'moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa mu Gehena, m'moto wosazima.


Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya ku Gehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo.


Kukolowekedwa mwala wamphero m'khosi mwake ndi kuponyedwa iye m'nyanja nkwapafupi, koma kulakwitsa mmodzi wa ang'ono awa nkwapatali.


monganso kwalembedwa, kuti, Onani, ndikhazika mu Ziyoni mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa; ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi.


Chifukwa chake, ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama kunthawi yonse, kuti ndingakhumudwitse mbale wanga.


Koma ine, abale, ngati ndilalikiranso mdulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo chikhumudwitso cha mtanda chidatha.


Ndipo, Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa. Kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa