Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 26:42 - Buku Lopatulika

42 Anamukanso kachiwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ichi sichingandipitirire, koma ndimwere ichi, kufuna kwanu kuchitidwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Anamukanso kachiwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ichi sichingandipitirire, koma ndimwere ichi, kufuna kwanu kuchitidwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Adachokanso kachiŵiri nakapemphera kuti, “Atate, ngati chikho chamasautsochi sichingandichoke, mpaka nditamwa ndithu, chabwino, zimene mukufuna zichitike.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Anachokanso nakapemphera kachiwiri kuti, “Atate anga, ngati chikhochi sichingandichoke, mpaka nditamwa, kufuna kwanu kuchitike.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:42
14 Mawu Ofanana  

Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza.


Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.


Ndipo anabweranso, nawapeza iwo ali m'tulo, pakuti zikope zao zinalemera ndi tulo.


Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.


Ndipo ananena, Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu; mundichotsere chikho ichi; komatu si chimene ndifuna Ine, koma chimene mufuna Inu.


nati, Atate, mukafuna Inu, chotsani chikho ichi pa Ine; koma si kufuna kwanga ai, komatu kwanu kuchitike.


Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.


Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa