Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 26:40 - Buku Lopatulika

40 Ndipo anadza kwa ophunzira, nawapeza iwo ali m'tulo, nanena kwa Petro, Nkutero kodi? Simungathe kuchezera ndi Ine mphindi imodzi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Ndipo anadza kwa ophunzira, nawapeza iwo ali m'tulo, nanena kwa Petro, Nkutero kodi? Simukhoza kuchezera ndi Ine mphindi imodzi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Atatero adabwerera kwa ophunzira aja, naŵapeza ali m'tulo. Tsono adafunsa Petro kuti, “Mongadi nonsenu mwalephera kukhala maso pamodzi nane ngakhale pa kanthaŵi kochepa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nawapeza ali mtulo. Iye anafunsa Petro kuti, “Kodi anthu inu, simukanakhala maso pamodzi ndi Ine kwa ora limodzi lokha?

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:40
12 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Kamuuzeni, Wakumanga zida asadzikuze ngati wakuvulayo.


Ndinagona tulo, koma mtima wanga unali maso: Ndi mau a bwenzi langa mnyamatayo agogoda, nati, nditsegulire, mlongo wanga, wokondedwa wanga, nkhunda yanga, wangwiro wanga. Pakuti pamutu panga padzala mame, patsitsi panga pali madontho a usiku.


Ndipo pamene mkwati anachedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo.


Petro ananena kwa Iye, Ngakhale ine ndikafa ndi Inu, sindidzakukanani Inu iai. Anateronso ophunzira onse.


Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa; khalani pano muchezere pamodzi ndi Ine.


Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.


Ndipo anabweranso, nawapeza iwo ali m'tulo, pakuti zikope zao zinalemera ndi tulo.


Ndipo anadza nawapeza iwo ali m'tulo, nanena ndi Petro, Simoni, ugona kodi? Unalibe mphamvu yakudikira ora limodzi kodi?


Ndipo pamene ananyamuka pakupemphera anadza kwa ophunzira, nawapeza ali m'tulo ndi chisoni,


Koma Petro ndi iwo anali naye analemedwa ndi tulo; koma m'mene anayera m'maso ndithu, anaona ulemerero wake, ndi amuna awiriwo akuimirira ndi Iye.


ndipo kukhale kuti m'mawa, pakutuluka dzuwa, muuke mamawa mugwere mzindawo; ndipo taonani, akakutulukirani iye ndi anthu ali naye, uzimchitira monga lidziwa dzanja lako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa