Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 24:39 - Buku Lopatulika

39 ndipo iwo sanadziwe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Ndipo iwo sanadziwe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Sadazindikire kanthu mpaka chigumula chidafika nkuŵaononga onse. Zidzateronso pamene Mwana wa Munthu adzabwera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 ndipo sanadziwe za chimene chikanachitika mpaka pamene chigumula chinafika ndi kuwamiza onse. Umu ndi mmene zidzakhalira pobwera kwa Mwana wa Munthu.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 24:39
18 Mawu Ofanana  

Ndipo zinaonongedwa zamoyo zonse zimene zinali padziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndipo zinaonongedwa padziko lapansi: anatsala Nowa yekha ndi amene anali pamodzi naye m'chingalawa.


Udzati, Anandimenya, osaphwetekedwa ine; anandikwapula, osamva ine; ndidzauka nthawi yanji? Ndidzafunafunanso vinyoyo.


Ukanena, Taonani, sitinadziwe chimenechi; kodi woyesa mitima sachizindikira ichi? Ndi wosunga moyo wako kodi sachidziwa? Ndipo kodi sabwezera munthu yense monga mwa machitidwe ake?


Wolungama asamalira mlandu wa osauka; koma woipa alibe nzeru yakuudziwa.


Chifukwa chake anatsanulira pa iye mkwiyo wake waukali, ndi mphamvu za nkhondo; ndipo unamyatsira moto kuzungulira kwake, koma iye sanadziwe; ndipo unamtentha, koma iye sanachisunge m'mtima.


Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo Iye adzabwezera kwa anthu onse monga machitidwe ao.


Ndipo pamene Iye analikukhala pansi paphiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?


ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.


Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.


Pomwepo adzakhala awiri m'munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa:


ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pamwala unzake; popeza sunazindikire nyengo ya mayang'aniridwe ako.


Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake.


Taonani, opeputsa inu, zizwani, kanganukani; kuti ndigwiritsa ntchito Ine masiku anu, ntchito imene simudzaikhulupirira wina akakuuzani.


Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;


Pakuti ichi aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mau a Mulungu;


Ndipo anadza pandunji pa Gibea amuna osankhika mu Israele monse zikwi khumi, nikula nkhondo; koma sanadziwe kuti choipa chili pafupi kuwakhudza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa