Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 21:44 - Buku Lopatulika

44 Ndipo iye wakugwa pamwala uwu adzaphwanyika; koma pa iye amene udzamgwera, udzampera iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Ndipo iye wakugwa pa mwala uwu adzaphwanyika; koma pa iye amene udzamgwera, udzampera iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 “Aliyense wogwera pa mwala umenewu, adzasanduka zidutswa zokhazokha. Ndipo aliyense amene mwalawu udzamugwere, udzangomutswanyiratu.”]

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 Amene agwa pa mwalawu adzadukaduka, ndipo amene udzamugwere udzamuthudzula.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 21:44
22 Mawu Ofanana  

Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye.


Udzawathyola ndi ndodo yachitsulo; udzawaphwanya monga mbiya ya woumba.


Chifukwa chake mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa chambuyo, ndi kuthyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa.


Pakuti mtundu ndi ufumu umene udzakana kukutumikira udzaonongeka; inde mitundu imeneyo idzasakazidwa ndithu.


Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndi amitundu onse a padziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao.


Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.


Ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi, pakumva mafanizo ake, anazindikira kuti alikunena za iwo.


Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.


Ndipo anthu onse anavomereza, ndi kuti, Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.


Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho;


Munthu yense wakugwa pamwala uwu, adzaphwanyika; koma iye amene udzamgwera, udzamupha.


Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa.


monganso kwalembedwa, kuti, Onani, ndikhazika mu Ziyoni mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa; ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi.


natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza machimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira chimaliziro.


Ndipo, Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa. Kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa