Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 21:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo anamyankha Yesu, nati, Sitidziwa ife. Iyenso ananena nao, Inenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo anamyankha Yesu, nati, Sitidziwa ife. Iyenso ananena nao, Inenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Ndiye adangomuyankha Yesuyo kuti, “Kaya, ife sitikudziŵa.” Apo Iye adati, “Nanenso tsono sindikuuzani kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Choncho anamuwuza Yesu kuti, “Sitikudziwa.” Pamenepo Iye anati, “Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wa yani umene ndichitira izi.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 21:27
19 Mawu Ofanana  

Kodi Mulungu adzaphunzitsa yani nzeru? Kodi Iye adzamvetsa yani uthengawo? Iwo amene aletsedwa kuyamwa, nachotsedwa pamawere?


Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, nachiritsidwe.


Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.


Ndipo m'mawa, Lero nkwa mphepo: popeza thambo lili la cheza chodera. Mudziwa kuzindikira za pa nkhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo ino, simungathe kuzindikira.


Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.


Nanga mutani? Munthu anali nao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito kumunda wampesa.


Munthuyu anayankha nati kwa iwo, Pakuti chozizwa chili m'menemo, kuti inu simudziwa kumene achokera, ndipo ananditsegulira maso anga.


Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;


Koma ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa