Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 21:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati mundiuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati mundiuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Yesu adati, “Nanenso ntakufunsani funso limodzi. Mukandiyankha, ndiye ndikuuzeni kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Yesu anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani funso limodzi, mukandiyankha, Inenso ndikukuwuzani ndi ulamuliro wa yani umene ndikuchitira izi.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 21:24
6 Mawu Ofanana  

Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


Ndipo m'mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?


Ubatizo wa Yohane, uchokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu? Koma iwo anafunsana wina ndi mnzake, kuti, Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye?


Ndipo Iye ananyamuka, naimirira. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani inu, Kodi nkulola tsiku la Sabata, kuchita zabwino, kapena kuchita zoipa? Kupulumutsa moyo, kapena kuuononga?


Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa