Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 21:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo m'mene adalowa mu Yerusalemu mzinda wonse unasokonezeka, nanena, Ndani uyu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo m'mene adalowa m'Yerusalemu mudzi wonse unasokonezeka, nanena, Ndani uyu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Pamene Yesu adaloŵa mu Yerusalemu, mzinda wonse udatekeseka, ena nkumafunsa kuti, “Kodi ameneyu ndani?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Yesu atalowa mu Yerusalemu, mzinda wonse unatekeseka ndipo anthu anafunsa kuti, “Ndani ameneyu?”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 21:10
14 Mawu Ofanana  

Ndaniyu akwera kutuluka m'chipululu ngati utsi wa tolo, wonunkhira ndi mure ndi lubani, ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?


Ndani uyu alikudza kuchokera ku Edomu, ndi zovala zonyika zochokera ku Bozira? Uyu wolemekezeka m'chovala chake, nayenda mu ukulu wa mphamvu zake? Ndine amene ndilankhula m'cholungama, wa mphamvu yakupulumutsa.


Ndipo Herode mfumuyo pakumva ichi anavutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye.


Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.


Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!


ndipo anati, nanena naye, Mutiuze muchita izi ndi ulamuliro wotani? Kapena ndani iye amene anakupatsani ulamuliro umene?


Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, Ndani Uyu alankhula zomchitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira machimo, koma Mulungu yekha?


Ndipo iwo akuseama naye pachakudya anayamba kunena mwa okha, Uyu ndani amene akhululukiranso machimo?


Ndipo Herode anati, Yohane ndinamdula mutu ine; koma uyu ndani ndikumva zotere za iye? Ndipo anafunafuna kumuona Iye.


Chifukwa chake Ayuda anayankha nati kwa Iye, Mutionetsera ife chizindikiro chanji, pakuti muchita izi?


Koma anati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;


Namuka iwo awiriwo mpaka anafika ku Betelehemu. Ndipo kunali pakufika iwo ku Betelehemu, mudzi wonse unapokosera za iwo; nati, Kodi uyu ndi Naomi?


Ndipo Samuele anachita chimene Yehova ananena, nadza ku Betelehemu. Ndipo akulu a mzindawo anadza kukomana naye monthunthumira, nati, Mubwera ndi mtendere kodi?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa