Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 20:13 - Buku Lopatulika

13 Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangane ndi ine pa rupiya latheka limodzi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangana ndi ine pa rupiya latheka limodzi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Koma mwinimunda uja adayankha mmodzi mwa iwo kuti, ‘Iwe, inetu sindidakubere ai. Kodi suja tinapangana ndalama yasiliva imodzi?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 “Koma iye anamuyankha mmodzi wa iwo nati, ‘Bwenzi, ine sikuti sindinachite chilungamo. Kodi sunavomereze kuti ugwira ntchito ndi kulandira dinari?

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 20:13
11 Mawu Ofanana  

Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?


Kodi muchiyesa choyenera, umo mukuti, Chilungamo changa chiposa cha Mulungu,


Chingakhale chiweruzo changa udzachithyola kodi? Udzanditsutsa kuti ndili woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe?


Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe.


Ndipo pamene adapangana ndi antchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza kumunda wake.


nanena kwa iye, Mnzangawe, unalowa muno bwanji wosakhala nacho chovala cha ukwati? Ndipo iye analibe mau.


Ndipo Yesu anati kwa iye, Mnzanga, wafikiranji iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namgwira Iye.


Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa